A Nankhumwa abweleranso ku court: Ati sanakondwe ndi mmene anawachosera mu chani cha DPP
Yemwe adali wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DPP kummwera, a Kondwani Nankhumwa, watengera chipani cha DPP ku bwalo la milandu, kutsutsana ndi kuchotsedwa kwawo m’chipanichi.
Malinga ndi owayimira a Nankhumwa, a Wapona Kita, a Nankhumwa adachotsedwa m’chipanichi mosatsata malamulo.
A Kita ati nkhaniyi idzamvedwa ndi oweruza mlandu ku bwalo lalikulu la milandu a William Msiska pa 12 mwezi uno.
A Nankhumwa adachotsedwa m’chipani cha DPP chifukwa chokhala nawo komanso kutenga mbali pa msonkhano wa komiti yayikulu ya chipanichi, NGC, omwe chipani chidati udalibe mdalitso wa chipanichi.
Follow and Subscribe Nyasa TV :