Ntchito yomanga zipinda zophunzirira 10 900 za pulayimale yayambika
Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera wakhazikitsa ntchito yomanga zipinda zophunzilira 10,900 komanso malo osinthira 1000 pansi pa ntchito ya MARP.
Polankhula pa mwambowu omwe ukuchitikira pa sukulu ya purayimare ya Chikololere Ku Dedza, Dr. Chakwera ati iyi ndi njira yoonetsetsa kuti ana akuphunzilira malo abwino msukulu za dziko lino.
Malinga ndi mtsogoleriyu ntchitoyi ayigwira ndi ndalama zokwana K150 biliyoni kwacha ndi thandizo lochokera ku banki yayikulu pa dziko lonse, itha chaka cha 2025 ndipo amanganso nyumba za aphunzitsi 10,000.
Mphunzitsi wa mkulu pa sukulu ya Chikololere a Bridget Nseteka wati ana amaphunzira pansi pa mtengo ndipo ntchitoyi ithandiza kuchepetsa vutoli.
Mkulu wa World Bank kuno ku Malawi a Hugh Ridell wati nzokhumudwitsa kuti ophunzira ambiri amasiyira sukulu panjira ndikukalowa banja.
Ophunzira okwana 1 million ndiwo akuyembekezeka kupindula kuchokera ku ntchito yomanga zipinda zophunzilira zokwana 10,900 zomwe zimangidwe ndi thandizo lochokera ku World Bank.
Malinga ndi a Ridell, pakadali pano, m’sukulu 60 pasukulu 100, ophunzira 90 amapezeka chipinda chimodzi chophunzilira ndipo ntchitoyi ichepetsa vutoli ndi theka.
Follow and Subscribe Nyasa TV :