MP Noel Lipipa wa DPP akuti zokamba za a Chakwera ndi zomwe zili mu bajeti zikusemphana

Phungu wa chipani cha DPP ku Blantyre City South Noel Lipipa wati zomwe anayankhula mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera mu SONA chaka chino ndi zomwe zili mu ndondomeko ya zachuma ya chaka chino mzosagwirizana komanso mzosatheka.

Lipipa:

Izi zadza pomwe aphungu akupitilizabe kuikapo ndemanga zawo pa ndondomeko ya za chuma ya chaka chino yomwe inapelekedwa ku nyumba ya malamulo ndi nduma yaza chuma Simplex Chithyola Banda.

Malingana ndi Lipipa, Unduna wa za chuma udasintha akadawulo  ma udindo osiyanasiyana mu unduna wu zomwe ati zili ndikuthekera kosokoneza kakonzedwe ka bwino ka ndondomeko ya za chuma yoyendetsera dziko.

Mwachitsanzo, Lipipa wati ndizodandawulitsa kuti boma likuikabe ndalama zochuluka pafupifupi 160 Billion Kwacha ku ndondomeko ya zipangizo zotsika mtengo za ulimi AIP yomwe ati sikubweretsa zotsatira zogwirika mdziko muno.

Kuonjezera apo Lipipa wati boma likuyenera kuika ndalama zokwanira bwino ku ndondomeko zomwe zingathandize dziko lino kumapanga Katundu osiyana siyana ku zokolora mkumatumiza ku maiko akunja zomwe zingamabweletse ndalama za maiko ena mdziko muno.

Mmawu ake, Lipipa mwazina wapempha boma kufunika koika chidwi komanso ndalama zokwanira ku ntchito monga za Migodi komanso zokopa alendo kuti zithandizire kupititsa patsogolo ntchito za chuma mdziko muno.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Primary School teacher in Dedza arrested for raping, impregnanting Std 7 pupil

Dedza Police have arrested Mtandamula Primary School Teacher Allan Medi for allegedly raping and impregnating a Standard 7 pupil. Nyasatimes...

Close