Ma Mega Farm ayambikadi: Kawale akhutisidwa ndi kupita patsogolo kwa Mlambe Mega Farm ku Mangochi

Unduna wa zaulimi wati ukupitiliza kukwanilitsa masomphenya a pulezidenti Lazarus Chakwera oonetsetsa kuti njala itheretu mdziko muno polima zakudya kudzela mu ulimi othilira.

Kawale kuyendera Mlambe Mega Farm

Izi anena ndi nduna ya za ulimi a Sam Kawale lero atayendera mmene ntchito yokonzaso Mlambe Mega Farm ikuyendela ku Nkopola, Mangochi.

“Mega Farm imeneyi ndi ya ma hekita 800 ndipo ma hekita 200 ndi amene tayamba kugwilitsa ntchito panopa ndipo tipanga ulimi othilira tikangokolola,” anatero a Kawale.

Iwonso anatinso kuti kuyamba mwezi wa mawa akangokolola chimanga chomwe chili mmunda kale, farm iyi iyambanso ulimi wina wamthilira mu mwezi wa May.

“Pamene tizithilira ma hekita 200, ma hekita ena 200 akhala akukonzedwa kuti tionjezele pa ulimi othilirawu, mpaka ma hekita 800 onse akonzedwe kuti tizikolola katatu pa chaka.

Malingana ndi a Kawale, Mega Farm imeneyi ikwanilitsa Masomphenya a 2063 mu njila ya ulimi wa makina (Mechanization), kukolola kangapo pa chaka (increased productivity), anthu 1,200 alembedwa ntchito (job creation), ndalama zambili zipezeka akamagulitsa mbewu (wealth creation) komanso kubweletsa ndalama zakunja tikagulitsa mbewu zimene akolole (forex generation).

“Zimene tikupanga ku Mlambe tikupanganso malo ena ambili mdziko lino. Tikuyesetsa kuthetsa njala ku unduna wanu wa Za ulimi polima minda ikulu ikulu (Mega Farms) komanso pogwilitsa ntchito mthilira,” atero a Kawale.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
UN, Lilongwe City Council collaborates in provision of hygiene materials at Area 13 market

In a collaborative effort to mitigate hygiene related diseases, the Lilongwe City Council (LCC) together with the United Nations(UN) donated...

Close