Boma la Dr Lazarus Chakwera awunikanso maphunziro ndi cholinga choti afanane ndi zolinga za Malawi agenda 2063
Boma la Dr Lazarus McCarthy Chakwera likusintha dongosolo la zamaphunziro ndi cholinga chakuti maphunziro adzifanana ndi dongosolo la ndondomeko ya boma ya Agenda 2063.
Izi zikutanthauza kuti m’malo moti ophunzira azikhala otanganidwa kuloweza ziwalo za ziwala iwo azitanganidwa ndi kuphunzira maluso osiyana siyana monga kakonzedwe ka magalimoto, kusoka zovala , kukhoma zidebe ndi maluso ena onse.
Mukulankhula kwawo pa msonkhano waukulu omwe wayamba pa 22 April , 2024 ku Mkopola ku Mangochi, Mlembi mu unduna wa za maphunziro a Dr Mangani Chilala Katundu, wanena kuti izi zikugwirizana ndi masomphenya a zomwe mtsogoleri wadziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera akhala akunena.
Pakadali pano mkulu wa Malawi Institute of Education (MIE) Dr Frank Mtemang’ombe watsimikiza kuti ndondomeko ya tsopanoyi ikhala ikugwira ntchito kuyambira chaka cha mawa.
Dr Mtemang’ombe watsindika kuti Kusintha kwa ndondomeko imeneyi ithandiza kutenga mbali yaikulu yokweza chuma cha dziko la Malawi.