Wapsa waku Israel: Achinyamata 500 anyamuka mu mwezi wa August
Achinyamata okwana 500 ndi omwe akuyembekezeka kunyamuka mwezi uno wa August kupita kukagwira tchito mdziko la Israel.
Mmodzi mwa akuluakulu ku unduna wa za ntchito a Paul Kalilombe wauza komiti ya Public Accounts ku nyumba ya malamulo kuti izi zili chonchi molingana ndi zomwe maiko a Malawi ndi Israel adakambirana posachedwapa. Iwo ati boma lapatsidwa mwayi oti kudzikolo kupite achinyamata okwan 3000.
A Kalilombe auzanso komitiyi kuti achinyamata omwe adamaliza kale ndondomeko za ulendo wawo kudzera mu kampani zomwe sizaboma {private recruitment agencies} akuyenera kulembetsanso ndi boma. Padakali pano, undunawu wati wayamba kale kulemba achinyamatawa sabata lino.