DPP isakunamizeni, a Malawi akuvutika chifukwa cha katangale wawo, watero Moses Kunkuyu

Mneneri wa boma a Moses Kunkuyu wati mavuto azachuma omwe dziko lino likudutsa pano ndi kaamba ka katangale yemwe anali ochuluka kwambiri mu nthawi ya ulamuliro wa chipani cha Democratic Progressive (DPP).

Poyankhula ndi imodzi mwa nyumba zofalitsa nkhani mdziko muno, Kunkuyu yemweso ndi nduna yazofalitsa nkhani, wati boma la MCP likukozaso ngodya zonse za dziko lino zomwe chipani cha DPP chidawononga.

“Amalawi adalipo ndipo alipo, aMalawi omwewo omwe adaona katangale wochuluka pansi pa ulamuliro wa DPP, alipo ndipo akuona komaso kusiyanitsa ndi zomwe zikuchitika pano.

“Boma likubwezeretsa ngodya zonse zomwe zidawonongeka ndi chipani cha DPP. Choncho sizoona kuti DPP idziti kuli mavuto pano chifukwa iwowo ndi omwe adapangitsa kuti kukhale mavuto pano,” watelo Kunkuyu.

A Kunkuyu ayankhula izi potsatira nsonkhano wa atolankhani omwe akuluakulu a chipani cha DPP anapangitsa Lachinayi munzinda wa Lilongwe komwe mwazina aloza chala boma kuti likulephera kuthetsa mavuto omwe akuta dziko lino.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Alumnus gives back to Mzuzu Govt Secondary School

A United States based alumnus for Mzuzu Government Secondary School (MZUGOSS), Vitumbiko Chiwaka, on Wednesday donated sports equipment and chrome...

Close