A Joyce Banda, a Muluzi, a APM auza mkulu wa polisi kuti amange anthu omwe anayambisa zipolowe ku Lilongwe

Omwe adakhalapo atsogoleri a dziko lino auza mkulu wa polisi a Merlyene Yolamu kuti afufuze komanso kumanga anthu omwe adachitira anthu nkhaza ndikuletsa zionetsero za zipani zotsutsa boma Lachitatu munzinda wa Lilongwe.

 

Atsogoleriwa, a Bakili Muluzi, a Joyce Banda komanso a Peter Mutharika, ati Amalawi akuyenera kupatsidwa mpata ochita zionetsero komanso kusankha atsogoleri akumtima kwawo mosaopsezedwa.

Iwo ati nzosavuta kupeza omwe adachita zachiwembuzi popeza pali kanema zomwe zikuonetsa nkhope zawo.

Atsogoleriwa auzanso President Lazarus Chakwera ndi chipani chake cha MCP kuti adzudzule zomwe zidachitikazi ndikutsimikizira Amalawi kuti izi sizidzachitikanso.

Mu kalata yawo, atsogoleriwa atinso bungwe loyendetsa chisankho la MEC komanso National Registration Bureau awunikire mavuto omwe akubala mpungwepungwewu.

“MEC iwunikirenso zogwiritsa ntchito kampani ya Smartmatic komanso zolepheretsa Amalawi kulembetsa mu kaundula wa voti kaamba kakulephera kwa NRB kupereka ziphaso zaunzika.

“Nthawi yochitapo kanthu ndi inoyi. Ulamuliro wathu wa demokalase umatero,” atsogoleriwa atero.

President Chakwera sadalankhulepo pa nkhaniyi pomwe mneneri wa MCP a Jessie Kabwila adauza otsutsa boma kuti abweretse umboni kuti ndi mamembala awo omwe adachita zauchifwambazi.
#TimesNkhani

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Subscribe
Notify of
guest

0 Comments
newest
oldest most voted
Inline Feedbacks
View all comments
0
Would love your thoughts, please comment.x
()
x
Read previous post:
First Lady Madam Chakwera donates relief food to Nkhota kota flood victims

First Lady Madam Monica Chakwera has donated 45 metric tonnes of maize flour and 5 metric tonnes of beans worth...

Close