A Kaliati awadzudzula kamba kobweretsa mpungwepungwe mchipani cha UTM

Mamembala achipani cha UTM omwe tinakwanitsa kucheza nawo adandaula ndi zochita za mlembi wamkulu a Patricia Kaliati kuti akuchita zodelera mtsogoleri wachipani chawo, a Dr Michael Biswick Usi.

Kaliati

Malingana ndi mamembala amenewa omwe sitiwatchula mayina, a Kaliati akhala akupanga ziganizo zochuluka pamodzi ndi anzawo ena mchipanichi zomwe sadafunse maganizo kwa mtsogoleri wachipanichi a Dr Usi.

Iwo ati izi ndi zomwe zikugawa chipani cha UTM. Malingana ndi mamembala amenewa, pali zitsanzo zambiri zomwe a Kaliyati akhala akupanga mosatsata malamulo. Iwo adapereka chitsanzo chochoka mumgwirizano wa Tonse Alliance kuti sadafunse maganizo a Dr Usi.

Iwo atinso Dr Saulos Klaus Chilima akadakhala moyo UTM sikadachoka monga Kaliati ndi anzake akufunira.

Titawafusa a Kaliati kuti ayankhepo pa izi iwo sadayankhe chilichonse pankhaniyi.

Pomaliza amene tayankhula nawo apempha a Kaliati kuti ayambe kupereka ulemu kwa a Dr Michael Biswick Usi chifukwa izi ndi zimene malamulo achipachi cha UTM amanena kuti mlembi wa chipani alibe mphamvu payenkha.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Analysis: Overall, APM performed well during last night interview with Times TV

The self-acclaimed CIA agent and DPP cadet, Foster F. Fundi , says I owe APM and all Malawians an apology...

Close