A Malawi aikila kumbuyo ganizo lopanga lamulo lomwe lidziletsa nkhalamba kuima pa chisankho

A Malawi ambiri omwe tayankhula nawo aikila kumbuyo ganizo lomwe anthu wena akhala akunena kuti pakhale lamulo lomwe cholinga chake ndi kuonenetsa kuti pakhale  malire a zaka zomwe munthu akuyenera akhale nazo kuti aime pa masankho a utsogoleri wa dziko lino.

 

Izi zikuchitika ngakhale zipani dzotsitsa boma zakhala zikukana ganizoli potengera kutimtsogoleri wawo kuchipani cha Democratic Progressive (DPP) ndi nkhalamba.

 

Isaac Banda yemwe ndi ochita malonda pa Area 23 wati ndi okondwa kuti akukhazikitsa lamulo longa ili.

 

A Banda adati, lamulo ili lithandiza kuti pampando tiziikapo munthu yemwe ali wamphamvu yekha yekha.

 

Naye Katswiri pankhani ya za malamulo Ayuba James , wayikira kumbuyo ganizo la phungu wa nyumba ya malamulo wa dera la lapakati m’boma la Mulanje  Kondwani Nankhumwa paganizo lomwe akufuna kuti nyumba yamalamulo ivomeleze kuti munthu akafika zaka 80 asamapikisane nawo pampando wautsogoleli wadziko lino.

 

Mmawu awo Katswiriyu Ayuba James wati ganizoli likavomelezedwa lithandiza kuchotsa anthu adyera omwe amafuna kukhala atsogoleri adziko lino ndicholinga chofuna kusakaza chuma cha dziko lino.

 

Iwo anaonjezelapo kuti ena mwa anthuwa amaononga ndalamazi kamba kakuti amadziwa kuti malamulo amateteza munthu wamkulu kusagamulidwa kukakhala kundende akapezeka olakwa pamlandu omwe wapalamula.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
DPP-USA Wing endorses Mutharika for 2025 presidential polls

The Democratic Progressive Party (DPP) United States of America (USA) Wing has endorsed the former Malawi President Professor Arthur Peter...

Close