Aford yasindika kuti izayima payokha ndipo yanenetsa kuti izatenga upulezidenti wa dziko lino
Chipani cha Alliance for Democracy (Aford) chati chili ndi chikhulupiliro kuti chidzapambana chikadzaima pa chokha pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko cha chaka cha mawa.
Wofalitsa nkhani za chipanichi a Amatullah Annie Maluwa auza Nyasatimes kuti kwa zaka zitatu tsopano chipanichi chakula mphamvu zimene zikupereka chirimbikitso kuti chidzaime pa chokha.
A Maluwa ati kutuluka kwa anthu ena mchipanichi ndi chitsimikizo kuti m’chipanichi muli demokalase ndipo anthu ena akhale akulowanso mchipanichi.
Posachedwapa, amene adali mlembi wamkulu wa chipanichi a Elias Wakuda Kamanga adatuluka mchipanichi ndi kulowa chipani chomwe chidayambitsidwa kumene cha National Development Party chomwe chikusogozedwa ndi a Frank Mwenifumbo
Aford inkadzudzula a Kamanga kuti ankapanga ndale za umthira kuwiri zomwe iwo eni adakana.
Follow and Subscribe Nyasa TV :