Bungwe la HRDC likuti iwowo ziwonetsero ayi, iwo asankha njira yokambirana ndi adindo
Bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lati layika chidwi chake pokambirana ndi adindo za mavuto omwe ali mdziko muno ndikupeza mayankho osati kuchita zionetsero.

Izi zadza pamene magulu ena okhudzidwa akonza zionetsero mzigawo zonse za dziko lino pa 10 mwezi uno kusonyeza kukwiya ndi momwe zinthu zikuyendera mdziko muno.
Mkulu oyendetsa ntchito zabungwe la HRDC Kelvin Chirwa wati kuti ndiufulu wa aliyense ofuna kuchita zionetsero koma kumbali yawo ngati HRDC akugwiritsa ntchito njira zina poyankhura ndi boma.
Mzaka za 2019 ndi 2020, moyendetsedwa ndi a Timoth Mtambo, bungweli linachilimika kutsogolera ziwonetsero mdziko muno zomwe zinawonongesa katundu wa anthu ambiri mdziko.
A Mtambo pano ali mchipani cha Aford atachotsedwa muboma la Tonse Alliance lomwe anali nduna yophunzitsa anthu.
Follow and Subscribe Nyasa TV :