Bungwe lobwerekesa ndalama la NEEF lapempha Akhristu mdziko muno kuti azibwedza ngongole
Bungwe la boma lobweleketsa ngongole la (NEEF) lapempha a khristu kuti adzibweza ngongole zomwe amatenga ku bungweli komanso mabungwe ena opereka ngongole.
Mmodzi mwa akuluakulu owona nkhanizi a Humphrey Thondolo, ndiye wanena izi Lamulungu madzulo pa mpingo wa Area 25 Assemblies of God pa maphunziro okhudza mene ndondomeko ya ngongole imayendera.
Malinga ndi a Thondolo maphunzirowa athandiza mamembala a mpingowu kumvetsetsa zokhudza ndondomeko ya ngongole.
M’busa wa mpingo wa Area 25 Asemblies of God Dr. Jim Bottoman Mbewe kubweza ngongole kaamba koti ndi mbali imodzi ya chiphunzitso cha chikhrisitu.
Membala wa mpingowu a Maud Gausi wati maphunzirowa abwera mu nthawi yake kutengeraso mavuto azachuma omwe akuta dziko lino.