Chakwera apempha a Malawi kuti asiye ndale zosungirana ka mpeni kumphasa
Mtsogoleri wa Dziko lino a Lazarus McCarthy Chakwera apempha a Malawi mdziko muno kuti asiye ndale zolozana dzala koma alimbikitse ndale zothandiza dziko.
A Chakwera anena izi pa Bwalo la Zamasewera la Chinsapo pamsonkhano wa chitukuko.
Asanapangitse msonkhano, a Chakwera adayendera kaye zitukuko zomwe zikuchitika mumzindawu.
Zina mwa zitukuko zomwe anayendera ndi mlatho wa ndalama zokwana K37Billion zomwe boma la Japan linapereka ku dziko la Malawi.
Komanso a Chakwera anayendera manyumba okhalamo anthu ogwira ntchito ya zachitetezo zokwana 90 zomwe boma likumanga kwa Chinsapo
Mmawu ake Mtsogoleri wadziko lino adatsimikizira a Malawi kuti iwo safoka ndipo sagwa ulesi ndi anthu omwe amamunena kuti sadapange chitukuko.
A Chakwera adati amadziwa kuti pali anthu wena omwe samayamika ndipo munthu utapanga chabwino chotani iwo amanyalapsa basi.
Chakwera wauza anthu kuti apitiliza kupanga ndale zothandiza a Malawi.
“Ndale zomwe ndikupanga ine
ndizopereka ulemu kwa ma bungwe aboma amene lamulo limawapatsa mphamvu zogwira ntchito mosapingika ndi anthu andale, ndipo sindisiya kutero chifukwa Pulezidenti
osalemekeza lamulo ndi ma bungwe aboma amakhala owononga dziko.
“Ndiye ineyo pempo langa lero ndiloti mundithandize kupanga ndale zotere, chifukwa ine mkuona kwanga, ndikuona kuti ndale zinazo sizitithandiza. Tonse tikudziwa kuti dziko lathu lachita ngozi zosiyanasiyana zomwe
zatisiya paululu waukulu. Dzanadzanalo tinachita ngozi ya Covid, yomwe mabala ake saanapole, ” adatero mtsogoleri wadziko lino.
Follow and Subscribe Nyasa TV :