Chakwera watsimikizira aMalawi kuti ngozi ya ndege ifufuzidwa mosabisa komanso mwapadera

Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus McCarthy Chakwera watsimikizira aMalawi ndi mayiko onse akunja kuti boma lake liwonetsetsa kuti ngozi ya ndege ifufuzidwa mosabisa komanso mwapadera pofuna kuti chilungamo chidziwike.

Chakwera wanena izi pa Bingu National Stadium mu mzinda wa Lilongwe pa mwambo wokhudza maliro a yemwe anali wachiwiri wake, Dr. Saulos Klaus Chilima.

Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu adamwalira Lolemba lapitali ndege imene anakwera pa ulendo wopita ku maliro a Ralph Kasambra itachita ngozi mu nkhalango ya Chikangawa.

Chakwera anati iye akudziwa kuti anthu ambiri ali ndi chikayiko ndi mmene ngoziyi idachitikira, choncho boma lake lipanga zothekera kuti kafukufuku achitike kuti anthu adziwe chilungamo.

“Ndikukutsimikizirani aMalawi nonse lero kuti ngozi imeneyi ifufuzidwa mosabisa komanso mwapadera. Ndawapempha kale amayiko akunja kuti atithandize kumbali imeneyi. Ndikudziwa kuti a Malawi Defense Force ali ndi ndondomeko yawo yofufuza kuti chinagwetsa ndege yawo ndi chani, koma kafukufuku wofunikira kwambiri ndi wopanga anthu ena apadera kuti aMalawi onse apeze mayankho okhulupirika, chifukwa nzosakwanira kuti MDF izifufuze yokha,” anatero mtsogoleriyu.

Chakwera anatsindika kuti monga aMalawi ambiri akufunsa za chomwe chidapangitsa ngoziyi, iyenso, monga kholo, nayenso ali ndi mafunso omwewo.

Iye anati ichi ndi chifukwa chake awapempha odziwa kafukufuku m’mayiko akunja kuti athandizire.

Koma mtsogoleriyu wapempha aMalawi kuti awawapatsa mpata ndi nthawi odzachita kafukufuku kuti agwire ntchito yabwino.

“Ngati tikufuna kafukufuku ameneyu ayankhedi mafunso athu, chonde pitirizani kusunga mtendere komanso kutonthozana mosunga bata. Koma ndikukutsimikizirani kuti kafukufuku wapadela ameneyu achitika ndithu, ndipo zotsatira zake zidziwika komanso zomwe zitapezeke kuti zinalakwika tiyesetsa kukonza,” anatero Chakwera.

Iwowo anapemphaso aMalawi kuti akhale achikondi kwa wina ndi mnzake pamene dziko likukhudza maliro a Chilima.

Chakwera anatsindika kuti maliro asakhale chifukwa chopangirana ma udani komanso kulakwirana.

“Mukulira kwathu sitilephera kulakwilana mmaganizo, mmayankhulidwe, ndi mmachitidwe, koma chonde tiyeni tisazitengere ku mtima chifukwa izi zimachitika chifukwa chaululu omwe tikusowa nawo chochita. Olo ine ndemwe ndikudziwa kuti ino ndinthawi yoti ndivomeleze kutukwanidwa ndikunyozedwa chifukwa kholo lomwe likuyenera kuvomereza kulira kwa aliyense ndi ineyo, ndiye chonde sindikufuna kuti wina abwezere mzake zowawa chifukwa cha amene asankha kuti kulira kwawo aphatikizemo mau ondipezera ine zifukwa. Olira sitimawatseka pakamwa, chifukwa mukuliramo Mulungu amakhalanso akutitonthoza ndipo ife mbali yathu ikhalenso kutonthozana osati kubwezerana zowawa, chifukwa nkhondo siimanga mudzi,” anatero.

Pokambapo za Chilima, Chakwera anati dziko la Malawi lataya munthu wofunikira kwambiri ndipo imfa imeneyi dziko liimva kuwawa nthawi yayitali chifukwa cha ntchito zabwino zomwe anachita zinakhudza anthu ambiri.

“Ngati pali chinthu chimodzi chimene ndinaphunzira kwa Dr. Saulos Klaus Chilima muzaka zinayi mmene ndakhala ndikugwira naye ntchito ndiubwino okhala munthu oleza mtima, munthu okhala bwino ndi aliyense, munthu osatengera zolakwa za ena kumtima, munthu osasunga mangawa, munthu osanyanyalira dziko lake, komanso munthu opilira pa nthawi yomwe zinthu zasokonekela,” anatero iyeyo.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Chakwera says he also has questions about the plane crash, assures of independent inquiry

President Lazarus Chakwera, who was leading a state funeral service for the departed Vice President, late Saulos Klaus Chilima, delivered...

Close