Chakwera wauza unduna wa zamaphunziro kuti uwunikenso ndalama za ophunzira ku koleji amalandira

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wauza Unduna wa Zamaphunziro kuti uwunikenso ndalama zomwe ophunzira mu sukulu za ukachenjede amalandira pamwezi kuti zikwezedwe.

A Chakwera ati ophunzira mu sukulu za ukachenjede asamasowe zofunikira pa moyo wawo monga sopo, kuti aziika chidwi chawo chonse pa maphunziro.

A Chakwera anena izi pa sukulu ya ukachenjede ya Malawi University Business and Applied Sciences komwe amakhazikitsa ntchito yotukula luso la a chinyamata pansi pa ndondomeko yotchedwa Unipod.

Mu chaka cha 2022 ndalamayi idakwezedwa kuchoka pa K200 000 kufika pa K350 000 pa chaka.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Ndale zonyoza sizitereka nsima – Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus McCarthy Chakwera wati ndi wokhumudwa ndi khalidwe la andale ena amene akulowetsa ndale pa...

Close