Chakwera wayamba kugawa chakudya kwa a Malawi osowa: Mabanja 1200 athandizidwa ku Mulanje

Ntchito yogawa chimanga ku mabanja omwe akhudzidwa ndi njala m’boma la Mulanje yayamba lero, lolemba kwa Mthiramanja komwe mabanja 1200 alandira chimangachi.

DC wa boma la Mulanje a David Kayiwonanga Gondwe ati mabanja 69,497 ndiwo alandire chimanga m’boma lonse la Mulanje kwa miyezi isanu m’bomali.

A Gondwe apempha anthu kuti apewe chisokonezo ndi ziwawa pa nthawi yomwe akulandira chimangachi.

Mmodzi wa anthu omwe alandira chimangachi a Stellia Mwanakomba a mmudzi wa Kululira ati thandizoli lafika pa nthawi yake pamene mnyumba mwawo munalibe chakudya chilichonse.

Malinga ndi lipoti la bungwe la Malawi Vulnerability Assessment Committee (MVAC), anthu 5.7 million ndiwo akhudziwa kwambiri ndi njala ndipo akufunika thandizo la chakudya.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Subscribe
Notify of
guest

0 Comments
newest
oldest most voted
Inline Feedbacks
View all comments
0
Would love your thoughts, please comment.x
()
x
Read previous post:
AFORD leader Chihana says cultural festivals are critical tools for uniting Malawi

President of the Alliance for Democracy (AFORD), Enoch Kamzingeni Chihana, has described cultural festivals as critical tools for promoting unity,...

Close