DPP yasosola mipando yambiri ya mankhasala ku Eastern Region
Wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha DPP mchigawo chaku mmawa a Bright Msaka wati ndiokondwa kuti chipanichi chatenga mipando yonse ya m’makhonsolo mchigawochi.
A Msaka ayankhula izi pambuyo pa chisankho cha wapampando wa khonsolo ya boma la Machinga.
Khansala Simplex Diwa wasankhidwa kukhala wapampando ndipo wachiwiri wake ndi khansala Davis Weja.
A Diwa ati awonetsetsa kuti ndalama za chitukuko zikugwira ntchito yake komanso kuti zitukuko zikutha mu nthawi yake.
A Diwa agonjetsa khansala Cidreck Standy wa chipani cha UDF yemwe anali pa mpandowu.