Ena aletsedwa kuyima ku konveshoni ya MCP

Pali kuthekera kwakukulu kuti anthu ena omwe angolowa kumene chipani cha Malawi Congress (MCP) sakapikisana nawo ku msonkhano waukulu wachipani-chi pamene komiti yomwe ikuyendetsa msonkhanowu ikuwunikira zikalata za opikisana.

 Kezzie Msukwa

Anthu omwe awonetsa chidwi kukapikisana nawo pa maudindo osiyana-siyana apereka zikalata zawo, koma komiti ikuwunika pofuna kupeza omwe ali ovomerezeka.

Nkhalapampando wakomiti yomwe ikuyendetsa zokonzekera za msonkhanowu, Kezzie Msukwa, wati komitiyi ikuwunguza zikalatazi ndipo mwa mfundo zina ndikuona zaka zomwe munthu wakhala m’chipani cha MCP, ndipo ati izi ndi malingana ndi NEC yachipanichi.

“Ife ngati komiti tiunikiranso mfundo yoti munthu kukapikisana nawo pa mpando waukulu ngati wakhala m’chipani kwa zaka zosachepera ziwiri,” watero Msukwa.

Ndipo katswiri pandale, Chimwemwe Tsitsi wati sakuona vuto pomwe wati mipando yotero chipani chikufuna kuti mukhale anthu omwe akudziwa mfundo zake.

Pakhala kusagwirizana pa mfundo yoti anthu omwe akuyenera kukapikisana nawo pa mipando ikulu-ikulu yachipani akuyenera kuti akhale mamembala achipani cha MCP kwa zaka zosachepera ziwiri.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Government, mining companies finally sign Mining Development Agreements-MDAs

Government through Ministry of Mining and Ministry of Finance has finally signed Mining Development Agreements (MDA) with Lancaster Exploration Limited...

Close