Joyce Banda ayamikila Chakwera kamba kolengeza kuti m’maboma 23 muli njala

Mtsogoleri wakale wadziko lino yemwenso ndi mtsogoleri wa Chipani cha Peoples Party (PP) Dr Joyce Banda, wayamikira mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera kamba kaganizo lake lolengeza kuti m’maboma 23 mwa maboma 28 ndi malo angozi zogwa mwa dzidzidzi maka kamba ka njala yomwe yakhudza madelaro.

Poyankhula pa bwalo la zamasewera ku area 23 mum’zinda wa LIlongwe , a Banda anati ganizo lomwe wapanga mtsogoleriyu lithandiza kuti maiko ndi mabungwe athandize dziko lino.

A Banda apempha a Malawi kuti athandize boma pankhani yothana ndi njala. Iwo adati kuthana ndinjala sintchito ya boma lokha ayi.

Pachifukwachi , a Joyce Banda adachenjeza a Malawi kuti asiye kunyoza boma mdzina loti labweretsa njala chifukwa nkhani ya njala yakhala yakhala ilipo.

Pakadali pano , a Joyce Banda apempha omwe amakhala akukangalika kunyoza boma kuti mmalo monyoza ayambepo kuthandiza.

“Akazabwera kuno ndikumati azapanga izi awuzeni apangiretu pano za mawazo ayi. Ine nchifukwa chake ndimapangiratu. Manyumba ndikumamanga pano, ” Adatero a Banda.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Despite economic turmoil, National Bank posts K120 bn profit

One of the leading Banks in the country National Bank of Malawi (NBM) plc has announced that they have made...

Close