Kamlepo wakwiya, ati ngati boma lipitilize kukondera asamukira ku Tanzania
Phungu wadera lakumvuma kwa boma la Rumphi a Kamlepo Kalua wati ndiwokonzeka kukhala nzika ya dziko la Tanzania ngati boma lipitilize kupereka ntchito za chitukuko mokondera.
Polankhula mnyumba ya malamulo masanawa a Kalua ati mzodandaulitsa kuti boma likuyenera kukwanilitsa malonjezano ake pa nkhani ya chitukuko kudera lawo pofotokoza kuti kuli mavuto mavuto ambiri.
Iwo ati Malawi ndiwa aliyense ndipo boma la a Chakwera lisamaone mtundu wa anthu kapena dera potukula dziko lino
Koma mtsogoleri wa zokambilana mnyumbayi a Richard Chimwendo Banda wati mzokhumudwitsa kuti a Kalua alankhula motere kaamba koti boma lakwanilitsa ntchito zosiyanasiyana za chitukuko kudera lawo komanso madera ena osiyanasiyana.