Katswiri akuti DPP siyonkhonzeka kulowa m’boma, kwachuluka zibwana
Katswiri olankhulapo pa nkhani zosiyanasiyana m’dziko muno Latim Matenje wati zomwe zikuchitika Ku nyumba ya malamulo maka ku mbali ya aphungu otsutsa a chipani cha DPP zikuwonetseratu kuti chipanichi sichili chikonzeka kulowa m’boma.
Malinga ndi Matenje, wapempha ma bwalo a milandu kuti abwere poyera ndikunena ngati atopa ndi kumva nkhani zokhuza chipani cha DPP kusiyana ndi kumangowapatsa ziletso zomwe zikukolezera mpungwepungwe ku chipanichi maka pa nkhani yokhuza yemwe akuyenera Kutsogolera a phungu otsutsa mu nyumbayi (Leader of opposition).
” Kuchedwetsa kwa milanduyi ndi gwero lomwe likupangitsa kuti anthu azikokanakokana Ku chipanichi chifukwa bwalo litati libwere poyera ndikuthetsa milanduyi zonsezi zitha kusiyika,” watero Matenje.
Chitsegulireni nyumba ya malamulo lachisanu sabata yatha, pakhala pali kusamvana pakati pa aphungu a chipani cha DPP komanso nyumbayi pomwe chipanichi chinasankha mayi Mary Navicha ngati otsogolera ku mbali yotsutsa mu nyumbayi pamene sipikala wa nyumbuyi a Catherine Gotani Hara anati nyumbayi ipitirira kuona a Kondwani Nankhumwa ngati otsogolera ku mbali ya aphungu otsutsa kufikira bwalo la milandu litathana ndi mavuto awo.
Pakadali pano, aphungu a nyumba ya malamulo a chipani cha DPP akuyembekezereka kuyankha zomwe mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera analankhula potsegulira nyumbayi (SONA) la chinayi.