Khoti lipereka chigamulo kwa a Chilima lero
Bwalo la High Court loona za milandu ya ndalama likuyembekezeka kupereka chigamulo chake ku Lilongwe 2 koloko masanawa pa mulandu wakatangale omwe akuyankha wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Chilima.
Chigamulochi chikhala chopereka chitsogolo ngati kuli koyenera kuti nthambi ya chitetezo ya MDF ipereke zikalata za maumboni ku bwaloli molingana ndi pempho la Chilima kudzera mwa omuimira pa mulanduwu.
Chilima akuganiziridwa kuti adalandira ndalama kwa mpondamatiki wina Zunneth Sattar kaamba kofuna kuti athandizire kupereka ma contract a boma mosatsata malamulo kwa chikhwayacho.
Mwa zina zomwe Chilima akufuna ndi zokambirana za pakati pa mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera ndi mkulu wakale wa asilikali Vincent Nundwe pa za contract ya Sattar zomwe MDF ikukana ponena kuti zikukhudza chitetezo cha dziko.
Chigamulochi chiunikira ngati umboniwu ulidi oika pa chiopsezo chitetezo cha dziko komanso ngati kuli kofunikira kuti mbali ya Chilima ikhale nawo podzagwiritsa ntchito kunena za kusalakwa kwawo.