Koma kumeneko!FDH Cup panopa yafika pa K150million kuchoka pa K120m
Banki ya FDH yakweza ndalama za mpikisano wa FDH Bank Cup kuchoka pa K120 million kufika pa K150 million.
Mkulu owona za malonda ku bankiyi, a Ronald Chimchere wanena izi kumwambo opereka mphoto kwa osewera komanso atolankhani amene adachita bwino mu mpikisanowu chaka chatha.
Pakadalipano, mwambowu uli mkati ku hotela ya Amaryllis mzinda wa Blantyre.
Ndipo katswiri wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets Patrick Mwaungulu ndi amene wakhala osewera wapamwamba kuposa aliyense mu mpikisanowu.
Wotchinga pagolo wa Mighty Mukuru Wanderers, William Thole
wapambana mphoto ya wotchinga bwino pagolo pomwe Zahaya Malitano wa Santhe Admarc FC wakhala osewera wongoyamba kumene koma yemwe adawonetsa luso lapamwamba.