Komiti yoona za malamulo ku Parliament yayi mulandu wa Paramount Holdings upitilire
Wapampando wa komiti yoona za malamulo Ku nyumba ya malamulo, Peter Dimba wati komitiyi yapeza kuti mlandu wokhudza Paramount Holdings Limited womwe wozenga milandu wa boma Masauko Chamkakala anawuthesa, upitilire.
Dimba wati komitiyi siinakhutitsidwe ndi chigamulo chomwe chinaperekedwa,pa mlandu womwe akulu akulu aku Paramount Holdings Limited inapereka zikalata zabodza Ku sukulu ya ukachenjede yomwe imagula njinga zamoto.
Pakadali pano Mkulu ozenga milandu mmalo mwa boma Masauko Chamkakala wakanitsitsa kuyakhulapo kwa olemba nkhani, zina mwa zomwe afokozera komiti ya nyumba-yi kufikira atamaliza kuyakha mafuso.
Lero ndi tsiku loyamba limene komiti ya aphungu yoyang’ana za malamulo ikulondoloza milandu yomwe ofesi ya ozenga milandu inaithetsa ku bwalo la milandu.
Komiti iyi yatinso yagwirizana ndi ganizo lothetsa mulandu wa katangale omwe wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino a Saulos Chilima amayankha.
Follow and Subscribe Nyasa TV :