Livingstonia Synod ipempha boma kuti lichose msonkho wapamalipiro a azibusa awo
Bungwe la Church and Society mu mpingo wa CCAP mu Synod ya Livingstonia, lapempha boma, ku bungwe lotolera misonkho la MRA, kuti lichotse msonkho wapa malipiro a azibusa a mpingowu.
Iwo ati ndi abusa a mpingo okhawu mu CCAP omwe amalipira msonkho wa PAYE pomwe anzizawo mu ma synod a Blantyre ndi Nkhoma satelo ayi.
Mkulu wa bungweli, mbusa Mc Bowman Mulagha, wanena izi pa msonkhano womva maganizo a anthu mchigawo cha ku mpoto pa ndondomeko ya za chuma ya 2024/2025, womwe wuli nkati mu mzinda wa Mzuzu.
A Mulagha ati azibusa amu Livingstonia Synod amadalira chopeleka cha anthu mu mpingowu kuti alandile malipiro awo, zomwe zisokwanila, komanso iwo ati azibusawa amavutika kwambiri makamaka myengo yino yomwe anthu amatanganidwa ndi za ulimi.
“Takhala tikulemba makalata ku boma pa nkhaniyi ndipo takhala tikuwakumbusanso mnjira zosiyanasiyana koma sakutithandiza. Chonde imvani kupempha kwathu,” watero mbusa Mulagha.
Another form of handouts, leaving a few of us with tax burden, am totally against this approach