Mabungwe a NAC, PMRA akhumudwa ndi kufala kwa mauthenga a bodza a mankhwala a HIV

Mabungwe a National Aids Commission (NAC) ndi Pharmacy and Medicines Regulatory Authority (PMRA) ati ndiokhumudwa ndi kufala kwa mchitidiwe ofalitsa mauthenga abodza okhudza matenda a edzi kudzera mmasamba a mchezo monga TikTok, Facebook komanso WhatsApp.

Wamkulu wa bungwe ka NAC, Mayi Beatrice Matanje wawuza atolankhani mu mzinda wa Lilongwe kuti kafukufuku wa posachedwa yemwe mabungwe a NAC ndi PMRA mogwirizana ndi nthambi ya Polisi anachita, wapeza kuti pali akamberembere ena omwe akumagula mankhwala odziwika mma pharmacy, kumatula/kuchotsa zolembedwa pa mankhwalawo ndi kumata ma sitika olemba kuti Gammora.

Mayi Matanje ati akambererewa akutsatsa mankwalawo nkumawauza anthu kuti ndi katemera wa mankhwala omwe amapheratu HIV.

Iwo ati mankhwala achinyengowa akumawagulitsa pa mtengo wa pakati pa K90,000 ndi K260,000.

” Dziwani kuti mauthenga achinyengowa ali ndi
kuthekera koika miyoyo ya anthu ochuluka omwe ali ndi HIV pa chiopsezo,” atero a Matanje.

Iwo akukumbutsa anthu onse mdziko muno kuti pakadali pano mankhwala a HIV sadapezekebe.Mankhwala omwe alipo ndi aja ama ARV omwe amathandiza kuti HIV isachulukane mthupi mwa munthu yemwe alinayo.

A Matanje awonjezera kuti kumwa ma ARV mwandondomeko kumachepetsa chiwerengero cha HIV kufika pa mulingo wakuti nthawi zina osapezekaso pamene munthu wapita kukayezetsa HIV yi kuchipatala.

“Anthu ena akumatenga zotsatira zoterezi ngati umboni wosonyeza kuti munthu wachila ku HIV pambuyo pakugwiritsa ntchito mankhwala achinyengowa a Gammora,” atero a Matanje.

Powonjerapo, Mkulu wa PMRA a Mphatso Kawaye wachenjeza anthu kuti kufalitsa uthenga wabodza okhuza HIV ndi Edzi ndi mlandu malingana ndi gawo 98 la PMRA Komanso gawo 25 la NAC.

“Aliyense opezeka akupanga, kuitanitsa kuchokera kunja, kapena kugulitsa mankhwala achinyengo akupalamula mlandu,” atero a Kawaye.

Iwo ati aliyense wopezeka akuchita chinyengochi adzayimbidwa mlandu ndikuyikidwa mndende kwa zaka khumi (10years) kapena kulipira chindapusa cha K10 million.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Economist hails plan to transport fuel through rail as Nacala Logistics responds to Chakwera’s call to revamp rail transport

Presidential aspirant and economist Milward Tobias has hailed a plan by Nacala Logistics, a concessionaire that operates the country's railway...

Close