Madam Chakwera ali ku Switzerland ku msonkhano wokambirana zothesa matenda a TB

Mayi wa fuko lino,Monica Chakwera yemwenso ndi kazembe pankhani yolimbana ndi matenda a chifuwa cha TB kuno ku Malawi akuyembekezeka kuyakhula nthumwi pa nkhani za umoyo zomwe zikusokhana  mdziko la Switzerland komwe ali nawo pa msonkhano  waukulu pa dziko lonse okambirana njira zolimbana ndi matenda a chifuwa cha  chachikulu cha TB (World Health Summit).

First Lady Madam Monica Chakwera 

Madam Chakwera  apita ku msonkhanowu atayitanidwa ndi bungwe la Stop TB Partnership ndipo akuyembekezeka kuyakhula ku msokhanowo lachitatu la pa 29 May.

 

Bungwe la Stop TB Partnership  ndi bungwe lomwe linakhazikitsa mgwirizano wa atsogoleri amayiko osiyana siyana kuti atsogolere ntchito yolimbana ndi matenda a TB mwezi wa September mchaka cha 2023 ku msonkhano waukulu wa mayiko onse omwe umachitikira  ku New York mdziko la America.

 

Malingana ndi kafukufuku wa bungweli amene anachitika mchaka cha 2022, anthu okwana 1.3 million ndiomwe anamwalira ndi matendawa pa dziko lonse lapansi ndipo mwa anthuwa 167,000 analinso ndi kachilombo ka HIV.

 

Kuno ku Malawi anthu okwana 26,000 ndiomwe anapezeka ndi matenda a TB mchaka cha 2021 ndipo mwa anthuwa, anthu okwana 3,000 anamwalira.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Darkness falls in Chiradzulu as teenager, 17, stabs teacher to death and injures another man

A 17-year-old boy has been arrested and is being held in custody for allegedly stabbing to death a 33-year-old teacher,...

Close