Mgawaniko walowa ku aphungu a UTM: Ena akuti akhala kumbali ya boma, ena akuti ayi

Aphungu a chipani cha UTM agawanikana mmene akufunira kukagwira ntchito mnyumba ya malamulo nkumano ukayambaika. Ena akuti sakufuna kukakhala mbali ya boma pomwe ena anenetsa kuti sachoka mbali ya boma.

Kwavuta ku UTM

 

Mtsogoleri wa aphunguwa mnyumbayi a Chrissie Kanyasho wanena kuti alembera kalata Sipikala wa nyumba ya malamulo a Catherine Gotani Hara kuwadziwitsa za ganizo lawo.

“Talemba kale kalata, ikupita kwa a Sipikala moti mawa akaipeza pa tebulo pawo,” atero a Kanyasho.

A Kanyasho ati, aphungu a UTM okwana asanu omwe ndi iwowo, a Steve Mikaya a Blantyre West, a Simon Salambula a Ntcheu West, a Felix Kayira a Karonga North West ndi a Chrispin Mphande a Nkhata Bay West ndiomwe akufuna kukakhala mbali yotsutsa boma.

Iwo atinso aphungu ena omwe adapambana ngati oima pawokha kenako nkulowa UTM okwana 6 nawo ati sakufuna kukakhalanso mbali ya boma.

Koma tamvetsedwa kuti aphungu ena omwe adapambana paokha nkulowa UTM akukana kuchoka kuboma.

Mmodzi mwa aphunguwa, a Biswick Million a Zomba Changalume wanenetsa kuti sachoka mbali ya boma.

A Kanyasho ati omwe akhalebe mbali ya boma akabwenze galimoto ya chipani, chifukwa ndiye kuti sakugwiranso ntchito ndi UTM.

“Chipani chathu chatuluka mu mgwirizano ndiye nafenso tikuchoka ku mbali ya boma mnyumba ya malamulo,” atero a Kanyasho.

Akuluakulu ku nyumba ya malamulo sadalankhulepo pa nkhaniyi.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
86-yr-old Mama Kadzamira tumbles in court as she got grilled over Mchinji farm

Thirty years after the fall of Kamuzu Banda's dictatorship and 46 years after he gifted his 'official hostess' a 580...

Close