MHEN ayiyamikila pa ntchito yopititsa pa tsogolo nkhani za umoyo

Gulu la amayi la Kawalika Mother Care Group (MCG), layamikila ntchito yomwe bungwe la Malawi Health Equity Network (MHEN) likugwila pophunzitsa za kufunika kwa akatemela osiyanasiyana omwe ana osapyola dzaka zisanu amayenela kulandila, ponena kuti izi zachepetsa imfa za ana achichepele-wa.

Wapampando wa gulu la amayi-wa Judith Nowa wanena izi pambuyo pa maphunzilo achibweleza (refresher trainings) omwe bungweli likuchititsa m’boma la Lilongwe ponena kuti nawonso azibambo akutha kuzindikila kufunika kwa akatemela-wa ndipo akutha kutenga nawo gawo potengela ana awo kuchipatala kukalandila katemela pomwe amayi adwala.

“Ife monga gulu la amayi tikuyetsetsa kumemeza za kufunika kwa akatemela amenewa, tikaona kuti m’mayi nzathu akufooka timamuyendela ndikukamulimbikitsa kuti ayesetse kutsata ndondomeko za akatemela onse,” Nowa anafotokoza.

Senior HSA pa chipatala cha Malembo, Edigar Kadzakalowa wati ntchito yakatemela ikuyenda bwino kusiyanitsa ndi kale popeza kubwela kwa MHEN kugwila ntchito limodzi ndi unduna wa za umoyo zathandiza kuti amayi ambili azindikile za kufunika kolandilitsa mwana akatemela onse mwandondomeko.

“Magulu amene MHEN yakhazikitsa kuno kwathu kwa T/A Khongoni akuthandizila kuti amayi-wa adzitha kukumbutsana za kufunika kolandilitsa mwana akatemela onse mwandondomeko potengela ndi zomwe akuphunzila kuno kotelo kuti izi zikupititsanso patsogolo ntchito yolandilitsa katemela kwa ana,” Kadzakalowa anayakhula motelo.

MHEN ndi thandizo lochokela ku Global Alliance for Vaccination and Immunization (GAVI) likuchititsa maphunzilo a chibweleza kwa magulu amayi omwe anakhazikitsidwa m’boma la Lilongwe kufuna kumemeza komanso kuphunzitsa amayi anzawo kufunika kolandilitsa mwana akatemela onse mwandondomeko.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Subscribe
Notify of
guest

0 Comments
Inline Feedbacks
View all comments
0
Would love your thoughts, please comment.x
()
x
Read previous post:
ACB admits it is failing to fight corruption, says ‘truth be told, corruption is worsening’

Despite various interventions to aid the fight against corruption, the Anti-Corruption Bureau (ACB) says graft continues to worsen in the...

Close