Mtengo was shuga wafika K2600: A Malawi adandaula ati athawire kuti?
A Malawi ambiri akulira mokweza kamba kakupitilira kwa kukwera mtengo wa zinthu monga packet la shuga lomwe madera ambiri likugulisidwa pakati pa K2400 ndi K2600.
Nyasatimes inayankhula ndi anthu osiyana siyana kuchokera m’mbali zosiyana mdziko muno ndipo ambiri akuwonesa kugonja ndi kuthodwa chifukwa katundu akukwerabe mtengo komanso katunduyo amapangidwa konkuno.
Koma mkulu wa kampani yopanga sugar mdziko muno ya Illovo Sugar, wati mtengo wovomerezeka wa shuga ndi K2000 koma anakana kuyankhulapo pa nkhani yoti ena akugulisa shuga pa mtengo was K2600.
Izi zikupangisa a Malawi ambiri kukhala onyinyirika kuti athawire kuti chifukwa ngakhale bungwe la boma loteteza anthu pa malonda, Competition and Fair Trading Commission, lati silinapangebe kafukufuku wofuna kudziwa mmene mitengo ya shuga ikuyendera.