Mulandu wa Bushiri awuimitsa mpaka pa July 17 akuti chifukwa otsogolera boma, a Malunda, adwala
Bwalo la Lilongwe chief resident magistrate laimitsa mpaka pa 17 July 2024 kumva mulandu omwe dziko la South Africa likufuna kuti mneneri Shepherd Bushiri ndi mkazi wawo apite mdzikolo kuti akayankhe milandu.

Kuimitsaku kwachitika kambakoti yemwe akutsogolera ma loya a mbali yaboma, a Dzikondianthu Malunda wadwala.
Lero, oimira a Bushiri amayenera kupitiliza kufunsa mafunso mboni yaboma a Sibongire Mzinyathi omwenso ndi mkulu waboma otengera milandu kubwalo lamilandu ku South Africa ko.
A Bushiri komanso mkaziwawo Mary dziko la South Africa likuwaganizira kuti amazembaitsa ndalama mdzikoli mwazina.