Mzaka zitatu zapitazi Chakwera wakhululukira akaidi oposa 8000

Nduna yoona za malamulo, a Titus Mvalo yati mtsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera wakhululukira akaidi oposa 8,000 kuchoka m’chaka cha 2020.


Iwo ati kukhulukira akaidiku ndi njira imodzi yochepetsera kuthithikana ndi mu ndende za dziko lino.

A Mvalo, omwe ndi wapampando wa komiti yomwe imaunikira nkhani zokhulukira akaidi, ayankhula izi atatsogolera komitiyi, kuona zomwe akaidi ku ndende yaikulu ya Zomba akukumana nazo.

Mwa zina, zinadziwika kuti pa ndende ya Zomba pali akaidi okwana 2,126 ngakhale ndendeyi inamangidwa kuti muzikhala akaidi 800.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Ernest Kaonga elected to double as Private Schools SACCO President

Days after being elected as Private Schools Association of Malawi (PRISAM) president, Ernest Kaonga, has yet again been elected to...

Close