Ndale zonyoza sizitereka nsima – Chakwera
Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus McCarthy Chakwera wati ndi wokhumudwa ndi khalidwe la andale ena amene akulowetsa ndale pa nkhani ya njala yomwe yagwa mdziko muno.
Polankhula m’mzinda wa Blantyre pomwe amatsegulira chipatala cha matenda a khansa cha International Blantyre Cancer Centre (IBCC), Chakwera wati akudziwa kuti andale ena adzimudzudzula iye ngati amene wabweretsa njala mdziko pamene kusintha kwa nyengo ndi kumene kwabweretsa vutoli.
“Koma ndikufuna ndikuunzeni kuti ndale zonyoza sizitereka nsima,” anatero mtsogoleriyu.
Chakwera anatsindikanso kuti boma lake ndi lodzipereka kugwira ntchito ndi wina aliyenda pothana ndi vuto la njala, ponena kuti mgwirizano ndi wofunikira kwambiri pa ntchito yothana ndi vuto la njala.
Iwo anati boma lawo lili mkati kugawa ufa kwa mabanja omwe akhudzidwa ndi njala pofuna kuti pasakhale wina aliyense akufa ndi njala pamene iwo ali pa mpando wa mtsogoleri wa dziko lino.