Ndimawawidwa mtima ndi umphawi wa akumudzi ndi achinyamata – Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus McCarthy Chakwera wati ndiwowawidza mtima komanso kukhudzika kwambiri ndi umphawi womwe aMalawi akumudzi komanso achinyamata amakumana nawo.

Chakwera wati ichi ndi chifukwa chake kuyambira pamene adasankhidwa kukhala mtsogoleri wa dziko lino, boma lake lidakhazikitsa masomphenya a Malawi 2063, omwe cholinga chake ndikukhazikitsa njira zochulukitsira chuma cha aMalawi.

Mtsogoleriyu wanena izi pamwambo wosangalalira ntchito yomwe bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) yagwira popereka ngongole za nkhaninkhani kwa ochita bizinesi osiyanasiyana mdziko muno.

Chakwera anati kaamba kowawidwa ndi kukhudzika mtima kumeneku, ndi chichifukwa chakenso pasanathe chaka chilowele m’boma, iye adapita kunyumba ya Malamulo kukawauza aphungu kuti akauze anthu awo zomwe boma lake lawakonzera.

“Ziinthu zomwe boma langa labwera kuzawachitira ndi zitatu, ndipo choyambilira ndikuwathandiza a Malawi kupeza chuma chawochawo. Umphawi ndi chinthu chozunza kwambiri, ndipo umphawi unakhazikika mMalawi muno kuyambira kalekale, ndipo pena munthu umadabwa kuti kodi umphawiwu kuti ufike sayizi imeneyi, anthu amene anali m’boma m’mbuyomu ankapanga chani?” anatero Chakwera.

Iyeyo anapitiriza kunena kuti ndi wokondwa kukhala nawo pa mwambo wochitira umboni kuti ntchito za NEEF zathandiza aMalawi kupeza chuma chawochawo mmene iye ankafunira.

Chakwera anauza nantindi wa anthu omwe adakhala nawo pa mwambo umenewo kuti awafunse aphungu awo a ku Nyumba ya Malamulo kuti ndi chifukwa chani akhala akuwonerera umphawi wawo.

“Ine ndiye mbali yanga nditha kuyankha, kuti muzaka folo ine boma langa lagawa ngongole zoposa 100 billion kwacha kwa anthu oposa 175,000 amene ayambitsa mabizinesi osiyanasiyana nkulemba ntchito anthu oposa 500,000 kudzela programu ya NEEF. Ineyo mbali yanga ndithat kukamba molimba mtima kuti ndipo pamenepa mpang’ono, chifukwa imeneyi inali fezi yoyamba chabe, chifukwa ndalama zomwe titagawe mu fezi yachiwiri muzaka folo zikubwerazi zikhala zoposa zimenezi. Onse amene mwakhala mukudikira kuti nanu tikuthandizenu takuikani mmaplani okufikirani mu fezi yachiwiri kuti zokoma zomwe akusimba aMalawi amene alandila ndalama zimenezi nanunso muzasimbe nawo. Ndiye ngati programu imeneyi ikuthandiza kuthetsa umphawi komanso kusintha miyoyo ya aMalawi motere, ine ndimati ndikufunseni mafunso,” analongosola chonchi mtsogoleriyu.

“Funso langa loyamba ndiloti, kodi ngati mMalawi muno muli anthu amene akudana ndi programu imeneyi yokupatsani inu aMalawi ndalama zopangila mabizinesi, tiziti anthu amenewo akukufunilani aMalawi zabwino? Funso langa lachiwiri ndiloti, kodi amene akumati boma la Chakwera liyimire panjira nkuthetsedwa, zomwe zitalepheretse aMalawi inu amene mukufuna zomwe tapanga ku NEEF zaka folo zapitazi nanu zikufikileni mu zaka folo zikubwerazi, tiziti amenewo akukufunilani aMalawi zabwino? Funso langa lotsiriza ndiloti, kodi zoti tigawe ndalama zina zankhaninkhani mu fezi yachiwiri ya programu ya NEEF mu zaka folo zikubwerazi, mukufuna zichitike kapena zisachitike?” anafunsa chonchi.

Chakwea anapempha aMalawi kuti asabwerere m’mbuyo komanso asalole kuti ena awadyere masuku pamutu povomereza kuti thumba la NEEF lidzasokenezedwe ndi andale adyera.

Chakwera anamemanso aMalawi kuti agwire ntchito pamodzi naye pofalitsa uthenga wa chikayiko komanso wonamiza aMalawi kuti mdziko muno sapindulamo kanthu.

“Ife tonse tizizungulira ndi uthenga wa chilungamo komanso wa chiyembekezo, uthenga owauza aMalawi zowona, kuti ntchito zowathandiza aMalawi kuti apeze chuma chawochawo zikutheka, ndipo amene sanafikilidwe nawo afikilidwa akapanda kukhulupira mabodza a wanthu omwe akungofuna awachenjelere. Inunso amene mukudziwa kuti munalandira ndalama ndipo zasintha moyo wanu, mufalitse uthenga wabwino kuti amene akudikila fezi yachiwiri ya programu ya NEEF nawo akhale ndi chiyembekezo. Chifukwa wina afune asafune, programu ya NEEF ipitilira ndipo ine sindisiya kukutumikirani inu amene munandituma kuti ndigwire ntchito yothana ndiumphawi wanu,” anatero iwowo.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Mgawaniko walowa ku aphungu a UTM: Ena akuti akhala kumbali ya boma, ena akuti ayi

Aphungu a chipani cha UTM agawanikana mmene akufunira kukagwira ntchito mnyumba ya malamulo nkumano ukayambaika. Ena akuti sakufuna kukakhala mbali...

Close