Nthambi ya zanyengo yati mvula iyamba February 1 ndipo igwa yambiri mwezi wonsewu
Nthambi yoona za kusitha kwanyengo m’dziko muno yati pali chiyembekezo chachikulu kuti mvula iyamba kugwa mawa pa 1 February m’zigawo zonse za m’dziko muno.

Wofalitsa nkhani Ku nthambiyi a Yobu Kachiwanda watsimikiza za izi ponena kuti zigawo zonse m’dziko muno zikuyembekezeka kuyamba kulandira mvula mwezi wa February.
“Madera ambiri akuchigawo chapakati komanso ummwera kwa dziko lino akhala asakulandira mvula kwa sabata imodzi koma kuyambila lachinayi mvula iyamba kutsika kufikira kumapeto a sabatayi,” atero a Kachiwanda.
Izi zikudza pomwe alimi m’dziko muno akhala ali kakasi ndi ng’amba yomwe inayamba kuwononga chimanga komanso mbewu zina zakumunda.