Phungu wa DPP a Suleman akufuna mkulu wa Immigration atule pansi udindo
Phungu wa nyumba ya malamulo wa Blantyre South East Sameer Suleman wati m’kulu wa Nthambi yoona za anthu otuluka ndi kulowa m’dziko muno (immigration) atule pansi udindo kamba koti palibe chomwe akuchita ndipo wakalamba.
A Suleman ati nzokhumudwitsa kuti mpaka pano ziphaso zoyendera sizikupangidwa zomwe zikusokoneza ntchito za a Malawi ambiri.
Iwo ati izi zikuchitika pomwe boma la Tonse likutumiza a chinyamata kupita Ku Israel, zomwe ati apita bwanji opanda ziphaso.