Phungu wa UTM Susan Dosi akuti: “Kodi nkachoka ku boma kupita ku opposition, zipindulira ndani?”
Phungu wa Chikwawa West a Susan Dossi, yemwe anawina ngati phungu oyima payekha kenako nkulowa UTM, wati chipanichi sichinamufikire ndi uthenga woti achoke ku mbali ya boma kupita yotsutsa boma.
A Dossi ati ngakhale chipanichi chitawafikira, sakuona phindu lochoka mbali ya boma chifukwa anthu kudera lawo akufuna chitukuko chomwe chimachokanso kuboma komweko.
“Kodi nkachoka ku boma kupita ku opposition, zipindulira ndani? Ine olo andiitane kuti akandiuze zoti tichoke, priority yanga ili pa anthu a dera langa omwe adandivotera kuti ndipite kunyumba ya malamulo kukagwira ntchito ndi boma kuti titukule Chikwawa West.
“Chifukwa tikachoka kuboma, tidzipemphanso boma lomwelo zitukuko ndiye ganizo limenelo silikundimvekera bwinobwino. Panopa, chomwe chili chofunika kwa ine ndi mseu komanso bridge ya Chikwawa-Chapananga ndi ma projects ena omwe anthu anga akufuna, zomwe zichoke ku boma lomwelo,” atero a Dossi.
Aphungu a UTM auza Sipikala wa nyumba ya malamulo kuti awasamutsire ku mbali ya boma pomwe zokambirana za nyumbayi zikuyamba mwezi wa mawa.
Mmodzi mwa aphunguwa a UTM, a Biswick Million a Zomba Changalume, nayeso anawuza Nyasatimes kuti wanenetsa kuti sachoka mbali ya boma.
Koma mtsogoleri wa chipani cha UTM kunyumba yamalamulo a Kanyasho ati omwe akhalebe mbali ya boma akabwenze galimoto ya chipani, chifukwa ndiye kuti sakugwiranso ntchito ndi UTM.
“Chipani chathu chatuluka mu mgwirizano ndiye nafenso tikuchoka ku mbali ya boma mnyumba ya malamulo,” atero a Kanyasho.