Tiyeni tigwirane manja pothana ndi mchitidwe ochitira ana nkhaza, watero Bushiri
Prophet Shepherd Bushiri watsindika kufunika kogwirana manja pothana ndi mchitidwe ochitira nkhaza ana ndi cholinga chokwanilitsa masomphenya a dziko lino pa chitukuko.
Mneneri Bushiri wanena izi masanawa pomwe amagula katundu osiyanasiyana wa mwana wa mmudzi mwa mndola Mfumu yaikulu Kambwiri m’boma la Salima yemwe anadyetsedwa dowe wamuwisi ngati chilango kwa iye.
Malinga ndi a Bushiri nkhani ya mwanayu ndiyomvetsa chisoni ndipo alonjeza kuti amuthandiza mwanayu ku nkhani ya maphunziro ake pomupezera sukulu yogonera konko.
Wina mwa katundu yemwe amugulira mwanayu ndi monga zovala,sapato komanso zofunda.
Anthu osiyanasiyana kuphatizikapo bungwe la Malawi Human Rights Commission (MHRC) adzudzula kanema yemwe wakhala akuzungulira mmasamba a mchezo osonyeza mwanayu akudyetsedwa dowe wamuwisi.
Follow and Subscribe Nyasa TV :