Usi akuti: “A Chilima pomwe amatisiya anali m’boma, ine ndili m’boma, ndiye zalakwika pati?”

Mtsogoleri wa chipani cha UTM Michael Usi, omwenso ndiwachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, wadzudzula mlembi wa chipani chawo, a Patricia Kaliati kaamba kolankhura mosaganiza bwino.

A Usi polankhura kwa otsatira chipanichi ku kunyumba ya boma ya Mudi anati uwu ndi mtudzu ndipo iwo salimbana nawo.

“A Chilima pomwe amatisiya, anali m’boma, ine ndili m’boma pofuna kutumikira zomwe a Chilimawo ankafuna, ndiye zalakwika pati?”

Dzulo pa msonkhano wa ndale ku Mzuzu, a Kaliati anati mamembala eni Eni a UTM ndikomwe anali pa msonkhano osati omwe akukakamila kukhala mboma.

Lero a Usi omwe ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino akuyembekezeka kutsiriza ntchito zawo m’chigawo chakum’mwera zomwe agwira sabata ziwiri.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
World Vision Malawi impressed with its sponsorship program

World Vision Malawi says the transformative journey they embark on seven decades ago through sponsorship program now they have started...

Close