Wanenetsa Chakwera! Ati iyeyo sazalema kusakasaka thandizo lotukulira a Malawi

Mtsogoleri wa dziko lino watsimikizira aMalawi kuti sadzatopa kusaka thandizo la ndalama zogwirira ntchito za chitukuko mmadera onse a dziko lino.

Chakwera wanena izi pamwambo wokhazikitsa ntchito yomanga misewu yomwe boma la Malawi ligwire ndi thandizo la ndalama kuchokera ku Millennium Challenge Compact II la mdziko la USA.

Iwo anaulula kuti pa ulendo wawo wopita ku America atangolowa m’boma, otsutsa adawadzudzula kuti akuyenda maulendo opanda phindo.

Koma akuti izi sizidawabwezere mmbuyo pa cholinga chawo chofuna kukapempha thandizo lotukulira dziko lino.

“Nthawi zambiri, kukhala Prezidenti kumafanana ndi kukhala kholo. Olo zolinga zako zikhale zabwino, umayenela ukhale okhonzeka kuti ubwino omwe ukumuchitila mwanayo, nkutheka kuti mwanayo akutukwana nawo ndikumakuona ngati oyipa. Mwa chitsanzo, ndindani mdziko muno amene ali kholo amene sakudziwa kuti mwana akadwala umayenela ulole kuti adane nawe pamene ukumubayitsa jakisoni wa katemela kapena wa mankhwala kwa adokotala? Ndindani mdziko muno amene ali kholo amene sakudziwa kuti adokotala akakupatsani mankhwala okammwetsa mwanayo, umayenela ulole kuti adane nawe pamene ukumubwatula kukamwa mokakamiza kuti amwe iye asakufuna?” anafunso chonchi mtsogoleriyu.

Chakwera anati ngakhale izi zimakhala chonchi, iwowo akuzindikira kuti ndikholo lopusa lokha lomwe lingapange chiganizo chosiya kumulandiritsa mwanayo ma jakisoni ndi mankhwala chifukwa choti mwanayo amamva kuwawa kapena chifukwa choti mwanayo saamafuna komanso amatha mau.

Iwo anati ichi ndi chifukwa chake atangolowa m’boma mchaka cha 2020, adawayimbira tenifolo bambo Sean Caincross, amene anali wamkulu ku Millenium Challenge Corporation, kuwauza zakufunika kwa miseu imeneyi, ndipo iwo anati a Prezidenti tiyeni tigwire ntchito limodzi kuti zitheke.

Chakwera anafotokozanso kuti ulendo wawo ku America mu March chaka cha 2022 unali ngati jakisoni chifukwa potengera phokoso limene ulendowu unabusa mdziko muno.

“Akuti musapiteko kumeneko aPrezidenti. Akuti ndalama zomwe mutayendele ulendowo zipita pachabe. Akuti tikudziwa kuti palibe chomwe mutakachiteko kumeneko. Akuti tikudziwa zomwe ziri mumtima mwanu, kuti mukupita kumeneko kuti mukadya ma alawansi. Akuti, Akuti, Akuti, Akuti. Phokoso longa mwana kubayidwa katemela. Koma ine monga kholo ndinapita, ndipo Mayi Alice Albright ndinakawafikila, ndipo tinagwirizana zochita. Patadutsa miyezi seveni, Mayi Alice Albright anandiitananso, amvekere aPrezidenti mapepala oyamba amgwirizano wathu uja tamaliza bwerani tizasayinilane, ndiye ine ndinanyamukanso, komatu ndiye munali phokoso la jakisoni wakunasale mdziko muno, koma ine ndinapita, ndipo tinasayinilana kuti boma la America litipatse ndalama zokwana 700 billion kwacha kuti timangile miseu imeneyi. Mwezi wathau amayi Alice Albright anandiitananso, amvekere aPrezidenti mapepala achiwiri amgwirizano wathu uja tamaliza bwerani tizasayinilane, ndiye ine ndinanyamukanso ulendo wachitatu wa ku nasale kukabayitsa mwana jakisoni, kulolela kutchulidwa mayina achipongwe,” anatero Chakwera.Sindidzalema kukusakira thandizo la zitukuko.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Malawi youthful entrepreneur Daniel Kwizombe launches Eka-Lite LED bulbs

Minister of Trade and Industry, Sosten Gwengwe, on Wednesday evening led local and international dignitaries at the launch of Eka-Lite...

Close