Zosamvetsetseka! Bambo amangidwa popereka mimba kwa mwana wawo wa zaka 14

Apolisi mu mzinda wa Blantyre amanga mkulu wina yemwe dzina lake ndi Wonderful Itikani wa zaka 41, kamba komuganizira kuti wappereka mimba kwa mwana wake wa zaka 14.

Malingana ndi Aaron Chilala Mneneri wa polisi ya Soche, Itikani akuganiziridwa kuti wakhala akuchita zogonana ndi mwana wakeyu kuchokera mchaka cha 2019 mpaka chaka chino.

Chilala mkuluyu ali ndi ana atatu ndipo ochitilidwa za chipongweyu ndi wachiwiri ndipo wakhala akumugona kuchokera pomwe anali ndi zaka khumi.

“Itikani, wakhala akutuluka mchipinda chake ndikukalowa mchipinda cha mwanayu mobisa ndi cholinga chokachita naye zogonana,” watero Chilala.

Pakadali pano, Chilala wati Itikani akuyembekezeka kukaonekela ku bwalo la milandu komwe akayankhe mlandu ochita zogonana ndi mwana wachichepere zomwe ndi zosemphana ndi gawo 138 la malamulo a zaupandu.

Itikani ndi wa mmudzi wa Kamtimbanya mdera la Somba ku Blantyre

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Good news as TB treatment success rate remains at 90% in Malawi

The National Tuberculosis (TB) and Leprosy Elimination Programme says Malawi is currently doing better as TB treatment success rates remain...

Close